Chewa translation

Ayah by Ayah

Tags

Download Links

Chewa translation translation for Surah At-Tahrim — Ayah 2

66:2
قَدۡ فَرَضَ ٱللَّهُ لَكُمۡ تَحِلَّةَ أَيۡمَٰنِكُمۡۚ وَٱللَّهُ مَوۡلَىٰكُمۡۖ وَهُوَ ٱلۡعَلِيمُ ٱلۡحَكِيمُ ٢
Ndithu Allah wakhazikitsa kamasulidwe kakulumbira kwanu, ndipo Allah ndiye Mtetezi wanu, Iye Ngodziwa kwambiri ndiponso Ngwanzeru zakuya (pa malamulo amene wawakhazikitsa kwa inu).1
Footnotes
  • [1] Mkazi ndimkazi basi. Mtumiki adanena m’Mahadisi kuti sipadapezeke mkazi amene ali wokwanira pa chinthu chilichonse kuyambira pamene dziko lidayamba mpaka kutha kwake kupatula akazi anayi basi. Iwowa ndi awa: Mayi Fatuma, Mayi Khadija, Mayi Mariya ndi mayi Asiya (mkazi wa Farawo). Kusakwanira kwa akazi pa chilichonse kumapezekanso ngakhale mwa akazi a Mtumiki, amamsautsa Mtumiki pomuchitira nsanje ngakhale kuti iwo amapemphera kwambiri, kawirikawiri makamaka amayi awiri awa Mayi Aisha ndi Mayi Hafsa monga momwe zilili m’ndime 4 ya sura iyi. Allah wawakalipira kwambiri m’ndime 5 ya sura yomweyi ndi m’ndime 28 ya surat Ahzab. Koma adalapa mwachangu ndipo Allah adawayanja monga zilili m’ndime 52 ya Sûrat Ahzab.