Chewa translation

Ayah by Ayah

Tags

Download Links

Chewa translation translation for Surah Ash-Sharh — Ayah 7

94:7
فَإِذَا فَرَغۡتَ فَٱنصَبۡ ٧
Basi, ukamaliza ntchito (yolalikira ndi Jihâd) limbikira kupemphera.1
Footnotes
  • [1] Tanthauzo lake nkuti: “Ukamaliza ntchito yako yolalikira kwa anthu zomwe Allah wakutuma kuti ulalikire, chita mapemphero ambiri. Umthokoze Mbuye wako pa chisomo Chake chimene wakudalitsa nacho.” Mneneri (s.a.w) adali kulimbikira kwambiri pochita mapemphero mwakuti amaima ndi kumapemphera kufikira miyendo yake kutupa. Amagwetsa mphumi pansi (sijida) mpaka kuganiziridwa kuti wafa chifukwa cha kutalika kwa nthawi yopempherayo.