Chewa translation

Ayah by Ayah

Tags

Download Links

Chewa translation translation for Surah Al-Bayyinah — Ayah 5

98:5
وَمَآ أُمِرُوٓاْ إِلَّا لِيَعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ حُنَفَآءَ وَيُقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤۡتُواْ ٱلزَّكَوٰةَۚ وَذَٰلِكَ دِينُ ٱلۡقَيِّمَةِ ٥
Ndipo sadalamulidwe (china) koma kuti ampembedze Allah (Mmodzi yekha) ndikuyeretsa chipembedzo chake popendekera ku choona (ndi kusiya njira zonama) ndi kuti asunge Swala ndiponso apereke chopereka (cha pachuma chawo); chimenecho (ndicho) chipembedzo choongoka.1
Footnotes
  • [1] Tanthauzo lake ndikuti “Mneneri uyu” sadadze ndi chinthu cha chilendo chakuti ndikumukanira. Koma iye akulamula za kupembedza Allah Mmodzi ndi kumuyeretsera chipembedzo Chake; kuima ndi kupemphera, kupereka chopereka ndi zina zotero. Zoterezi ndizonso adali kuphunzitsa aneneri onse omwe adadza ndi zipembedzo zoongoka.