Chewa translation

Ayah by Ayah

Tags

Download Links

Chewa translation translation for Surah Al-Ahzab — Ayah 26

33:26
وَأَنزَلَ ٱلَّذِينَ ظَٰهَرُوهُم مِّنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ مِن صَيَاصِيهِمۡ وَقَذَفَ فِي قُلُوبِهِمُ ٱلرُّعۡبَ فَرِيقٗا تَقۡتُلُونَ وَتَأۡسِرُونَ فَرِيقٗا ٢٦
Ndipo adawatsitsa m’malinga mwawo amene adathandiza adaniwo mwa anthu a buku (Ayuda). Ndipo adathira mantha m’mitima mwawo. Ena mumawapha; ndipo ena mumawagwira.1
Footnotes
  • [1] Awa ndi Ayuda amene adasakanikirana ndi osakhulupilira (akafiri) a Chiarabu ochokera mu mtundu wa Banu Quraidhwa omwe adali ndi mapangano ndi Mtumiki (s.a.w) okhalirana mwa mtendere. Koma pamene adaswa mapangano pothandizana ndi adani a Mtumiki kuthira nkhondo Asilamu Mtumiki Muhammad (s.a.w) adawapitira ku malinga awo. Ndipo ena adawapha, pomwe ena adawagwira monga akaidi a pankhondo.