Chewa translation

Ayah by Ayah

Tags

Download Links

Chewa translation translation for Surah Al-Ahzab — Ayah 49

33:49
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا نَكَحۡتُمُ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ ثُمَّ طَلَّقۡتُمُوهُنَّ مِن قَبۡلِ أَن تَمَسُّوهُنَّ فَمَا لَكُمۡ عَلَيۡهِنَّ مِنۡ عِدَّةٖ تَعۡتَدُّونَهَاۖ فَمَتِّعُوهُنَّ وَسَرِّحُوهُنَّ سَرَاحٗا جَمِيلٗا ٤٩
E inu amene mwakhulupirira! Mukakwatira akazi okhulupirira, kenako ndikulekana nawo musadawakhudze, inu mulibe chiwerengero cha ‘Edda’ pa iwo choti nkuchiwerengera. Asangalatseni powapatsa cholekanira. siyananawoni; kusiyana kwabwino.1
Footnotes
  • [1] ‘Edda’ ndi nthawi imene mkazi amakhala pa chiyembekezero asanakwatiwe ndi mwamuna wina pambuyo posiyana. Edda zilipo za mitundu iwiri: yosiyana ukwati yomwe mkazi amayembekezera miyezi itatu ndi yomwalira mwamuna yomwe mkazi amayembekezera miyezi inayi ndi masiku khumi. Koma mkazi wapakati Edda yake imatha ndikubereka. Yang’anani ndemanga ya Qur’an ( 2 : 228 ).