Chewa translation

Ayah by Ayah

Tags

Download Links

Chewa translation translation for Surah Saba — Ayah 2

34:2
يَعۡلَمُ مَا يَلِجُ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا يَخۡرُجُ مِنۡهَا وَمَا يَنزِلُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ وَمَا يَعۡرُجُ فِيهَاۚ وَهُوَ ٱلرَّحِيمُ ٱلۡغَفُورُ ٢
Akudziwa zimene zikulowa m’nthaka ndi zimene zikutulukamo; ndi zimene zikutsika kumwamba ndi zimene zikukwera kumeneko. Ndipo Iye Ngwachifundo kwabasi, Ngokhululuka kwambiri.1
Footnotes
  • [1] M’ndime iyi Allah akutidziwitsa kuti akudziwa zonse zimene zikulowa m’nthaka monga madzi, mitembo ndi zina zotero. Ndipo akudziwanso zimene zikutuluka m’menemo - monga mmera tizirombo, miyala yamtengo wapatali ndi madzi. Ndi zomwe zikutsika kumwamba monga mvula, matalala, mphenzi, madalitso, angelo Ake ndi mabuku Ake. Ndipo akudziwanso zimene zikukwera kumwamba - monga ntchito za akapolo Ake ndi zina zotero.