Chewa translation

Ayah by Ayah

Tags

Download Links

Chewa translation translation for Surah Fussilat — Ayah 12

41:12
فَقَضَىٰهُنَّ سَبۡعَ سَمَٰوَاتٖ فِي يَوۡمَيۡنِ وَأَوۡحَىٰ فِي كُلِّ سَمَآءٍ أَمۡرَهَاۚ وَزَيَّنَّا ٱلسَّمَآءَ ٱلدُّنۡيَا بِمَصَٰبِيحَ وَحِفۡظٗاۚ ذَٰلِكَ تَقۡدِيرُ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡعَلِيمِ ١٢
Choncho adakwaniritsa kulenga thambo zisanu ndi ziwiri mmasiku awiri, ndipo thambo lililonse adalidziwitsa ntchito yake (polilamula zochita zake). Ndipo tidakongoletsa thambo lapafupi (ndi inu) ndi nyenyezi (zounikira dziko lapansi), ndiponso kuti zizilondera kumwamha (kuti ziwanda zisamapite kukamvera za kumwamba). Uwu ndi muyeso wa Mwini mphamvu, Wodziwa kwambiri.