Chewa translation

Ayah by Ayah

Tags

Download Links

Chewa translation translation for Surah Fatir — Ayah 6

35:6
إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ لَكُمۡ عَدُوّٞ فَٱتَّخِذُوهُ عَدُوًّاۚ إِنَّمَا يَدۡعُواْ حِزۡبَهُۥ لِيَكُونُواْ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلسَّعِيرِ ٦
Ndithu satana ndi mdani wanu; choncho mchiteni kukhala mdani. Iye amaliitanira gulu lake kuti likhale gulu la anthu a ku Moto.1
Footnotes
  • [1] Allah watifotokozera kuti satana ndi mdani wathu wakalekale; iye ndi amene adatulutsitsa tate wathu Adam m’Munda wa mtendere pomulakwitsa. Ndipo iye adalumbira kuti adzapitiriza kutisokeretsa.