Resources
Tools
Docs
Community
FAQ
Github
Login
CMS
Resources
Tools
Docs
Credits
Community
FAQ
Github
Login
Developer Resources
Translations
Chewa translation
Chewa translation
Ayah by Ayah
Tags
Translation
Chichewa
chewa
nyanja
Download Links
Download simple.json
Download simple.sqlite
Preview
Docs
Licence
A translation of every ayah of the Quran in Chichewa, Chewa, Nyanja.
Chewa translation translation for Surah Ash-Shams — Ayah 11
Jump to Ayah
[]
← Previous
Next →
91:11
كَذَّبَتۡ ثَمُودُ بِطَغۡوَىٰهَآ ١١
Thamud (Samudu) adakanira (Mneneri wawo) chifukwa cha kulumpha malire kwawo.
1
Footnotes
[1]
(Ndime 11-15) Asamudu atchulidwa m’surat AL-FAJR. Anthu awa adamukana Mtumiki wawo, Mtumiki Swalih (a.s); adamuuza kuti ngati afuna amukhulupirire, atulutse ngamira kuchokera mthanthwe, apo ndipo adzamukhulupilira kuti ndi Mneneri. Swalih adampempha Allah, ndipo lidasweka thanthwe lija ndikutulukamo ngamira monga momwe adafunira anthu aja. Koma sadamukhulupirirebe. Mneneri Swalih (a.s) adawauza kuti: “Chenjerani ndi ngamira ya Allah iyi, musaikhudze ndi choipa chilichonse.” Ndipo adawakakamiza kuti pa tsiku limene ngamira ija ikumwa madzi, iwo asatunge madzi. Ndiponso pa tsiku limene iwo akutunga madzi ngamira siidzamwa madzi. Koma adamkanira. Ndipo m’modzi wa iwo amene adali wamphulupulu adaipha ngamira ija. Allah nthawi yomweyo adawatsitsira chilango chifukwa cha machimo awo, chomwe chidawakwanira onse kuyambira uja wopha ngamira ndi ena onse.
Loading…
Loading…